Kukongola wa Akazi Abstract

Nyanja
Maganizilo, kupenya, ndi kukamba Kwa Azungu  kuja kwa kupatula ndi kunyoza anthu a Cifirika ndi abale abo aba alikukhala kunja kwa dziko kwakhala kuli cucitika panthawi zaka 200. Cocititsa manyazi kwambili ndi maganizo ndi kukhulupira kwa Azunguwa kwakuti akazi a ciFirika kapena a mu Zambia emene azola mafuta bakuti ayeretse thupi bali ndimtima wozinyoza cifukwa afuna kuni khungu labo likhale monga lija la mkazi muzungu. Nkhani yimene nalemba yikuti pali njira yina yopambana mwamene tionera nkhaniyi. Nkhani iyi yikuti pali kuyika pamozdi ndi kuvundulila kayendelo ka thupi la munthu ndi mwambo-nkharo yamunthu ndi zimene zimapanga pa ife banthu umu timaonera za kukongorola kwa mkazi. Aka kaonero kathu kamasiyana kwambiri ndikaonero ka Cizungu kamene kamapenya ndi maso akupatula ndi kunyoza anthu a ciFirika ndi a muZambia. Nkhani iyi yosusa ndi kutenga mboni kucokera mmene anthu a ciFirika ndi mu Zambia amacongera za kukongola kwa akazi kulingana ndi kuyera-kufiyira ndi kuda kwa khungu la mkazi. Nkhani iyi yikutiso kuti mumene anthu ife timacongera akazi tingafufuze ndi kuvomeredzedwa pa aChewa, aBemba, aLozi, aTonga, aKaonda ndi mitundu yonse mu Afirika, cingakhare cabwino. Kaoneredwe aka, maganizo, ndi kukamba uku kungamatsule ndi kupasa ufulu kwa ife anthu aFirika amene tinaphunzira nzeru ndi sukulu ya Cizungu. Ife tonse tiri mu Afirika ndi kubwalo kwa ziko tingayambe kupenya kwa tsopano za kacongoredwe ndi kunyadila kwa kukongola kwa akazi akuda mcalo conse.

 

MAU AKULU

Anthropology ya Kukongola, Akazi ndi Amuna, Kukongola kwa akazi a CiFirika, kupatula banthu pakhungu labo, Anthu akuda ali kunja kwaziko, mwamo-nkharo ya ciFirika.

Leave a Reply

This site uses Akismet to reduce spam. Learn how your comment data is processed.